ZOTSATIRA
Njira Yophunzitsira mu Pulojekiti ya WITH:
Maphunziro apamwamba komanso olunjika pa ophunzira, adzapangidwa pachotsatira ichi. Chidziwitso chokwanira, luso, zikhalidwe ndi malingaliro zidzapangidwa molingalira ntchito zokopa alendo ndi cholinga chothandiza azimayi achichepere m'maiko a SSA kuti apambane ngati amalonda ndi eni mabizinesi a zokopa alendo.
Pulogalamu Yophunzitsa Aphunzitsi mu Pulojekiti ya WITH
Kuthandiza aphunzitsi kupeza chidziwitso chokwanira kuti athe kuthandiza amayi achichepere kukweza maluso awo a zamalonda komanso luso lawo laukadaulo pa ntchito zokopa alendo.
Gulu la akadaulo la WITH
Gawo ili ndi chotsatira ichi chizathandiza azimayi achichepere (zaka 18-35) pa maphunziro a mu pologalamu ya WITH kudzera mu kulumikizana (pakati pa okhudzidwa ndi pulojekitiyi, kuphatikiza azimayi ochita bizinesi ndi eni mabizinesi) ndi mgwirizano kapena kulumikizana pakati pa akadaulo (mwachitsanzo: maphunziro apamwamba a pa intaneti operekedwa ndi akatswiri komanso azimayi amalonda ochokera ku mayiko a EU ndi SSA; maulendo achionetsero ku makampani ndi mabizinesi akumayiko a SSA; misonkhano ya azimayi amalonda ndi eni mabizinesi m'mayiko a SSA; kukumana kwapadera, pakati pa mayi ochita malonda ndi alangizi m'maiko a EU kuti apange malingaliro abizinesi kapena mipikisano yamabizinesi;